13/01/2022
Munthu wina wachuma atasuzumira pa windo anaona Garden boy wake akutchetcha panja.
Ndipo iye anati Zikomo Mulungu pondipatsa Chuma!
Naye Garden boy anamva kugogoda atatuluka anapeza munthu wina akudzafunsira ntchito.
Ndipo naye anati oooooo Mulemekezeke MULUNGU pondipatsa Ntchito yi ena akuisowa.
Naye ofuna ntchito uja.
Akuyenda anaona Olumala akupempha.
naye anati..Oooo Mulungu wanga zikomo Pondilenga wangwiro ndiwamphavu mukwezeke.
Naye olumara uja anaona Wamisala Akudya zamu bini zoola zili ntchentche zokha zokha.
naye anati oooo!
Thanks God popeza sindili wamisala ngati uyo Mulemekezeke.
Patangotha 5mins naye Wamisala anaona Ambulance ili magesi thwani thwani ikuthamangira kuchipatala.
naye anathokoza Mulungu oooo Zikomo Namalenga ngakhale ndimadya zakubini koma sindidwala ndikudziwa kuti ndi mphanvu zanu.
Apapa kuti tionesese aliyense akuthokoza zimene Namalenga amamuchitila inu mumuthokoza motani?
Tayenda njira zosiyana,zipatala zosiyana siyana ndipo tadya zakudya zoti azathu ena anafa nazo koma ife osafa mpaka kuzalowa chaka chanyuwanichi tiyeni tonse pomwe tilipo tizimthokoza Mulungu
Nane ndingoti Zikomo Mulungu wanga pondpatsa Moyo wathaz ndiwangwiro!.
AMBUYE AZIKUDALITSANI NONSE NTHAWI ZONSE AMEN