LIMAC

LIMAC Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from LIMAC, Grocers, Lilongwe.

26/12/2023

Sibasi Christmas ija yatha ena atenga matenda ena kuvulazidwa ena kumwalira kumene nkhani yake Christmas bas zathapo tiyen tizilima Basi osamazitengera kwambiri

12/12/2023

.
Mkudziwa izi
1. Mamuna yemwe sanagonanepo ndi mkazi aliyense amatchedwa k*ti 👉🏿"Chaste" kapena "innocent" kapena "celibate" Kapenanso "Virginal" pomwe mkazi yemwe sanagonanepo ndi mamuna aliyense amatchedwa k*ti "virgin"

2. Madzi otentha amauma mwachangu akaikidwa mu fridge kusiyana ndi ozizira

3.madzi ozizira amatentha mwachangu mukawaika pamoto kusiyana ndi madzi omwe ndi ofunda kale

4.mkango waukulu bwino, pa chaka umapha nyama zosaposera 20
(Ine ndine Mzungu Wakuda)

5. Mkango umadya nyama yosachepera 5 kgs komanso yosaposera 7 kgs, ndipo ukadya nyama yotereyi umatha kukhala masabata atatu usadadyenso ina.

6. Njoka za mmadzi, kamba wa mmadzi, Ng'azi, Whale, Ng'ona komanso bokho, zinthuzi zimabanika komanso zimafa ngati zakakamizika kukhala nthawi yaitali mmadzi osaturutsa mutu.

7. Ng'ombe zimatha kugona zili chiimire, koma zimalota zikagona chogona.

8..khutu lilironse la mphaka, linakonzedwa ndi minyewa/minofu 32.

9. Mnyewa/Mnofu umene uli mu kamwa la munthu, ndi mnyewa omwewonso unapanga maliseche a mkazi(vagina)

10. Mu chaka cha 2003, katswiri wina otchedwa *Dr. Roger Mugford* adakonza kachida kotchedwa “wag-o-meter” kamene kamafotokonza nyengo (mood) ya galu pongoyeza kagwedezedwe ka mchira wake.

11. pa zolengedwa za Mulunguu, ndi nkhono yokha yomwe imati ikachotsedwa diso limameranso lina.
Pangani like pageyi k*ti muzitsatira zambiri zosangalatsa...
Pangani share k*ti anzanu adziwe nawo..

2023 Allow me to advice you freely

03/12/2023

Mulibwanji alimi azanga?Ndafuna ndigawane nanu mwaulere kapangidwe ka manyowa a mbeya, thumba la 50 kg la fertelizer kupangira matumba 5 ya manyowa mkudzakolora phwamwamwa.
PEZANI ZINTHU IZI
(1)Phulusa 10 kgs
(2)Manyowa ankhuku/Yankhumba 10kgs
(3)Gaga 10 kgs
(4)Fertelizer 10kgs
(5)Mkodzo 10Ls/madzi
KAPANGIDWE
*Sakanizani zonsezi bwinobwino zisapange phala kwambili zikhare pamulingo wabwinowabwino kenako thilani mu msaka la pepala mkati , njatani kukamwa kwake zisungidwe kwa masiku 21 kenako dzamasuleni mkuzikhuthula pamthuzi k*ti zipite mphepo , zikakamuka kufika pamulingo wak*ti zikhoza kumakathilika bwino basi mukhoza kukathira.
KATHILIDWE
*Tea spoon kapena chitsekelero cha fanta, chonde osachulutsa coz zimakhara zamphamvu kwambili.
*Usagundikizitsa ku nyemba pothilapo.
CHENJEZO
*Pomasula mu msakamo patatha masiku 21 chonde asamasule ndi mzimayi oyembekezera chifukwa m'pweya wake umakhara owopsa umatha kumuchotsa mimba mzimayi nthawi zina.
CHOWONJEZERA!
*Ngati mukupanga manyowa okulitsa onetsetsani k*ti mwachulutsako fertelizer wa NPK , m***a k*thilako 8kgs , urea 2kgs.
*Obeleketsa chulutsani Urea kenako 2kgs NPK.
Gwilitsani ntchito upangiliwu ndipo simudzakhumudwa, anthu asakubeleniso ndalama, ndapeleka upangiliwu mwaulere kwa inu ngati mphatso ya chikondi changa pa inu, ndimakukondani.
Muthaso kupanga forward kwa azizani k*ti nawoso apulumutse makwacha ndi kukoloraso zochuluka.
Ambuye amakukondani!
Ndikufunilani ulimi wopambana.
AMBUYE AKUDALITSENI
Osaiwara kupanga follow imeneyi k*t MALANGIZO A ulimi asakuphonyeni

Address

Lilongwe

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when LIMAC posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category