Ankadziwandani fukochinema Agama

Ankadziwandani fukochinema Agama Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Ankadziwandani fukochinema Agama, Grocers, Malawi, Balaka.

Ena amkafusa kuti kodi bungwe la ADRA limapanga chiyani , nanga eni wake ndindani ?Yankho bungwe limeneli ndi la katolik...
26/11/2024

Ena amkafusa kuti kodi bungwe la ADRA limapanga chiyani , nanga eni wake ndindani ?

Yankho bungwe limeneli ndi la katolika ,koma linapatsidwa kumpingo wa SDA ,pouthokoza mpingowu kuti unakwanilitsa popanga nawo mgwilizano ndi papa Ku Vatican ,

Bungwe limeneli amene amalithandiza ndi papa ,bungweli limalimbikitsa kukonza makondomu ,ndikumalimbikitsaso anthu awo akhilisitu awo kugwilitsa ntchito makondomuwa ,

Mwa ichi mafuso mkumati kodi makondomu ndi ofunikila kwa mkhilisitu ?

Mu zeni zeni ayi ndithu uku ndikulimbikitsa kuti anthu adzikonda kupanga chigololo ,zomwe ndi Mulungu ndi kutali kwambili ,

Komatu mumpingomu malamulo alipo ndithu akuti usachiche chigololo koma zimawonetsa kuti zimangolankhulidwa koma osachita ,zomwe zimawonetsela kuti ,

Kayimidwe ka mpingo wa SDA ndikakugwa ndithu chifukwa ndizosatheka mpingo kumalimbikitsa za makondomu ayi ,

Zachisoni zina mzakuti ndale ,ndi chikhilisitu ndi zinthu ziwili zosiyana ,koma zomwe zili apa mzakuti wamkulu wa bungwe ili ndi manganya amene ali wachiwili kwa pulezident wadziko lino ,

Ndiye izi zowopsya kwambili ena timadabwa kuti ndichifukwa chiyani Mtsogoleli wa mpingo wa SDA kuno Ku Malawi bwanji amakondana ndi chakwela pulezident wadziko lino?

Yankho mlakuti kuseliko adagwilizana koma anthu amawabisila ,izi mzofunika kwa munthu amene ali ndi ganizo lofuna kupulumuka akuyenela kutsekulapo maso ake ,ndikuchitapo kanthu ,

Kodi khisitu ndi Beliyali agwilizana bwanji ????

*MFUNDO ZOFUNIKA ZOKHUZANA NDI CHIPHUNZITSO CHA UTATU*✍️✍️✍️Lingaliro la Utatu mu Chikhristu linasintha kwa zaka mazana ...
26/11/2024

*MFUNDO ZOFUNIKA ZOKHUZANA NDI CHIPHUNZITSO CHA UTATU*

✍️✍️✍️Lingaliro la Utatu mu Chikhristu linasintha kwa zaka mazana angapo, kuyambira ndi Akhristu oyambirira omwe anazindikira umulungu wa Yesu ndi Mzimu Woyera pawokha posatengera malemba ngakhale kuti poyamba sanagwiritse ntchito mawu oti *"Utatu*".
✍️✍️✍️Tertullian (c. 160–225 AD) anali m'gulu la anthu oyamba kufotokoza momveka bwino ganizoli, kupanga mawuwa muzolemba zake motsutsana ndi mipatuko.
✍️✍️✍️Msonkhano wa ku Nicaea mu 325 AD unatsimikizira umulungu wa Khristu koma sunafotokoze mokwanira Utatu; izi zinakonzedwanso pa Msonkhano wa ku Constantinople mu 381 AD, umene unakhazikitsa kufanana kwa Mzimu Woyera ndi Atate ndi Mwana kuwapanga onse akhale Mulungu.
✍️✍️✍️Chiphunzitsocho chinapitirizabe kusinthika kudzera m’mikangano yazaumulungu, yosonkhezeredwa ndi utatu wachikunja wakale ndi malingaliro anzeru, zomwe zinapangitsa kufalikira Kwa Chiphunzitso chimenechi mu ma Middle Ages.

*Zipembedzo zachikunja zomwe zimakhala ndi lingaliro la Utatu zikuphatikizapo*:
1️⃣Chihindu:
👉 Trimurti ya Brahma, Vishnu, ndi Shiva imayimira chilengedwe, kusungidwa, ndi chiwonongeko, ngakhale chitukuko chamtsogolo

2️⃣Chipembedzo Chakale cha ku Aigupto:
👉 Utatu monga Osiris, Isis, ndi Horus amapereka chitsanzo cha mabanja aumulungu.

3️⃣Chipembedzo Chachiroma:
👉Utatu wa Jupiter, Juno, ndi Minerva unali wofunika kwambiri pa kulambira kwachiroma.

✍️✍️✍️Zipembedzo zamakono zachikunja zimene zimaloŵetsamo zikhulupiriro za Utatu kaŵirikaŵiri zimachokera ku miyambo yakale imeneyi koma pophatikiza kungoimasuliranso mwamakono. Zitsanzo zikuphatikizapo mitundu ina ya *Wicca ndi Neopaganism,* yomwe imavomereza lingaliro la mulungu wamkazi katatu pamodzi ndi chithunzi cha mulungu.

22/07/2024
14/07/2024


Chipani cha Malawi Congress (MCP) chabwela poyera ndikunena kuti sichikugwedezeka ndizomwe chipani cha UTM chanena kuti chatuluka mu mgwirizano wa Tonse Alliance, pomwe kwangotsala chaka chimodzi kuti chisankho chichitike.

Komiti ya Central Executive ku UTM yalengeza lachisanu kuti yachita chiganizo chotuluka mu mgwilizano ponena kuti siikuonatsogolo lili lonse. Koma komiti yaikulu NEC ikuyenera iunike ndikuvomeleza chiganizochi .

Poyankhulapo pa nkhaniyi, mlembi wa mkulu wa chipani cha MCP Eisenhower Mkaka wati kutuluka kwa UTM mu mgwirizano ndi kodandaulitsa koma sikukutanthauza mathero a boma la mgwilizanoli ponena kuti zipani zina zikanali ndi chikhulupiliro mu mphamvu ya mgwilizano.

(by John-Paul Kayuni – Lilongwe: 07/13/24)

Address

Malawi
Balaka

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Ankadziwandani fukochinema Agama posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category