Zachitika kutizoseketsa

Zachitika kutizoseketsa Contact information, map and directions, contact form, opening hours, services, ratings, photos, videos and announcements from Zachitika kutizoseketsa, Grocers, Dedza280, Dedza.

04/12/2024

M'malawi ndi munthu olimbikira kwambiri samatopa ayi or amwalire umuona uyo wasanduka fisi kumaba mbuzi🤣😂🤣😂🤣😂🤣😂🤣😂🤣😂

Masiku sakoma onse. Ndiliti limakomalo?
30/11/2024

Masiku sakoma onse. Ndiliti limakomalo?

30/11/2024

Mau akulu amakoma akagonera.ndinadya dzulo akukomadi

Kodi Bea ndikufuna ndikuuze kuti chibwezi chatha chifukwa  ndiwe oumila.Pangani follows page yathu ya   kutizoseketsa
30/11/2024

Kodi Bea ndikufuna ndikuuze kuti chibwezi chatha chifukwa ndiwe oumila.

Pangani follows page yathu ya kutizoseketsa

28/11/2024

Banja ndimavuto.mayi ako anakapanda kukwatilana ndi Bambo ako unakabadwa iwe? Mwakula sizonamizila kuti mu banja muli mavutozo😂😂😭😭

28/11/2024

Pangani follows page yathu dinani 👇👉 kuti mudziva zomwe zikuchitika mdziko muno

Nthambi yowona zanyengo ndi kusintha kwa nyengo mdziko muno yati mvula ya mphamvu ndi yamabingu ikuyembekezereka kugwa m’madera ambiri kuyambira lero lachinayi pa 28 November kufikira loweluka pa 30 November 2024.

Nthambiyi yati izi zili chonchi kaamba ka dera losakhanzikika la mkumano
wa mphepo zakumpoto komanso zakumwera omwe umatchedwa ITCZ.

Mwa zina nthambiyi yati derali likuyembekezereka kuyambira kumwera pa 28 November 2024 ndikumafalikira m’zigawo za pakati ndi kumpoto.

Malingana ndi nthambiyi madzi angasefukire m'madera omwe ngalande zake ndizotsekeka kapena zosalongosoka.

Mvula yomwe ikuyembekezereka ili ndi kuthekera kochititsa madzi kusefukira maka m’madera omwe ali ndi Chiopsezo cha kusefukira kwa madzi. Choncho, pofuna kupulumutsa katundu ndi miyoyo,nthambiyi ikuchenjeza anthu kukhala tcheru powonetsetsa kuti apewe kuwoloka malo omwe madzi akuthamanga kwambiri

Kukhala tcheru maka m’madera omwe madzi amasefukira pafupi pafupi,Kupewa kuusa mvula pansi pamitengo, Kubisala m’malo otetezedwa pomwe mphezi zikuomba m’dera awo.

Nthambiyi yati ipitiriza kuchita kalondolondo ndi kudziwitsa mtundu wa a
Malawi pa za kayendedwe ka kanyengo ku Malawi kuno.

(Wolemba: Hope Nyondo)

Address

Dedza280
Dedza

Website

Alerts

Be the first to know and let us send you an email when Zachitika kutizoseketsa posts news and promotions. Your email address will not be used for any other purpose, and you can unsubscribe at any time.

Share

Category