17/06/2026
*Chibwenzi chongoyamba kumene — titani kuti chikule bwino?*
Mwezi 1-3 yoyambirira ndi yofunika kwambiri. Ndi nthawi yomanga maziko kapena kuwononga zonse. N**i zoyenera kuchita:
*1. Musathamange — dziwanani pang'onopang'ono*
Chikondi chenicheni simoto wa udzu. Osafulumira kunena "ndimakukonda", kusamukira limodzi, kapena kukonza ukwati. Tengani miyezi 3-6 mudziwane kaye.
*Chifukwa*: Anthu ambiri amabisa makhalidwe oipa mwezi woyamba. Zoona zimatuluka pakapita nthawi.
*2. Ikani malire anu momveka bwino kuyambira tsopano*
Uzani mnzanu msanga:
- "Sindimakonda kutukwanidwa ngakhale titakwiya"
- "Ndimafuna kuti tizitumizirana message tikachedwa"
- "Sindikufuna kugonana mpaka titakwatirana/tikhale serious"
Anthu okhazikika amalemekeza malire. Osadikirira mpaka mwezi wa 6.
*3. Mufunseni mafunso ofunika, osati zosangalatsa zokha*
M'malo mongofunsa "Umakonda nyimbo yanji?", funsani:
- "Kodi banja labwino ndi lotani kwa iwe?"
- "Umatani ukakwiya kwambiri?"
- "Zolinga zako za zaka 5 zikubwerazi ndi ziti?"
- "Umagwirizana bwanji ndi banja lako?"
Mayankho ake akuwonetsa ngati muli ndi njira imodzi.
*4. Yang'anani zochita, osati mawu okha*
Aliyense anganene "Ndimakukonda" pa sabata yoyamba. Koma:
- Kodi amasunga lonjezo? Akati "Ndikuyimbira 8pm", amayimbiradi?
- Amalankhula bwanji ndi anthu osauka? Ndi operekera zakudya?
- Amachita bwanji akakhumudwa?
Makhalidwe ang'ono akuwonetsa mtima weniweni.
*5. Musabise umunthu wanu weniweni*
Anthu ambiri amadziyesa "angwiro" poyamba, kenako mtima weniweni umatuluka. Kuyambira tsopano khalani wekha. Ngati umakonda kuphika, phika. Ngati umakonda kupemphera, pemphera. Munthu woyenera adzakukonda chomwecho.
*6. Dziwitsani abwenzi ndi banja lanu msanga*
Chibwenzi chobisika nthawi zambiri chimakhala ndi vuto. Patatha mwezi 1-2, muuzeni bwenzi lanu lapamtima. Abwenzi amawona zinthu zomwe chikondi chimakupofulitsa. Ngati akukana kudziwitsidwa kwa anthu, funsani chifukwa.